24/10/2023
BAMUSI AKONDWA MOPITILILA MUYESO
apa ndikuti bamusi ali pa khomo lake ndipo iye anali kusesa pakhomo kamba ka matenda a kolera omwe anali kusawutsa mu mdera chifukwa anthu anayamba kuchita chimbudxi ma tchire chifukwa mu mderali dothi lake linali la mchenga .kotelo anthu anayamba kunyalanyaza zokumba zimbudzi chifukwa dzimangoloshoka kamba kamchengawu.
Ndipo patatha masabata angapo matenda anafika pofalikira makomo ambiri mu mderali ndipo ogwira mzake mkono amasowa ndipo bamusi anali munthu ekhayo mu mderali yemwe anakwanitsa kumanga chimbudzi chapamwamba chomwe chinali chokwanila popewa matendawa .
Ndipo zitafika pogwila makosi mikoko yogona inakhala pansi nukambilana zina mwa njira zomwe zingathetse matendawa mwachagu .koma atakambirana funo zawo bambo chikhosi omwe anali nduna ya amfumu amu derali anafuwula kwa mfumu nawawuza kuti pali bungwe lina lomwe lingathetse muriliwu powamangila zimbudzi ndipo bungweli anali kulitcha pamodzi tingathe kuthetsa mavuto.ndipo ndunayi itafokoza za bungweli onse anagwilizana nazo ndipo anapanga chothekela kuti bungweli libwere ndikuzathetsa vutoli .
Ndipo kenaka bungweli linabwera ndikudzayamba kupanga chitukukochi ndipo bamusi panthawiyi anali kuda nkhawa kamba ka muliriwu potengengela .za chithandizo chomwe anali kupeleka kwa achibale omwe anawasiya kumudzi kwawo.
Ndipo bamusi atava za bungweli anasangalala kwambili pozindikila kuti nkhawa zake zatha zomwe zinali kumusayutsa pa nthawiyi ndipo oye analowa mnyumba mwake natulutsa gumbagumba yake ndikuyika nyimbo inali kuvutitsa ma sipikala mu mderali yotchedwa simangeni anapita kwawo ndipo iye anathyola dasi yomwe aliyese anali kudabwa ndimomwe bamusi anali kuvinila ndipo sizinamukhudze chifukwa anavina tsache lili manja mpaka thukuta lomwe linanyowetsa zovala zake zonse kamba ka dzuwa lomwe linali kuwomba panthawiyi
Tsatilani kuti zambili zisakuphonyeni