08/07/2026
Anyani ndi Mulimi🐵🌽.
M'mudzi wina munali mulimi wina amene amalima chimanga kwambili 🌽, koma kumundako kunali ndi vuto limodzi kunali anyani ambili 🐵🐵. Zimene zimamupangitsa kuti assamagone, deyile amakhalila kuthamangitsa anyani maka ikakwana thawi yokolola🌽.
Koma akakolola amasiya mbali imodzi kussiyila anyaniwo🐵, koma nawonso anyani samakhutila🐵.
Nde anyani atawona kuti sakumadya momassuka, anaganiza zongomupha nkuluyi 😞, anayitanana nkuuzana plan ndipo onse anakhutila nayo 😁.
Nde kutacha Tsiku lotsatila mwini munda ananyamuka ulendo okadika anyaniwo, koma zachisoni😥 samadziwa plani yanyani adja, atangofika kumunda nkukhala pang'ono, anadabwa kukubwela nsambi wa anyani 🐵, anayesela kuwathamangitsa koma palibe chinathandiza ndipo anyani kunali kumakanda kanda 😞, kumukhadzula , muthu anayesela kukuwa koma palibe chinathandiza 🙆😞. Mpaka mulimi udja anafa 😥.
Anyani anasangalala kuti pano adzingodya mwawufulu, ndipo chaka chimenecho chinatha ali m'ma Happy.
Chaka chotsatila anyani 🐵, adja amachoka m'muthengo kupita kumunda kudja, koma zachisoni samapeza chimanga oro mbeu iliyose yomela yoti angadye😥😥.
Mpamene anazindikila kuti, munthu timadana naye udja😥, ndi amene amatisamala😥🐵, koma chifukwa cha umbuli apa tadzipha tonkha😥.
Mphunzilo:
Ambili pano tili ngati anyani amene timangofuna zithu zophweka😥😥, mpaka timapha abale athu, cholinga tikhale ndi chuma, koma chuma chidja chikatha mpamene timakumbukila kufunikila kwawo😥🐵.
Choonde kondani adani anu angakhale azanu poti chokudza mawa sichimadziwika😥.