09/02/2020
GENESIS 42:26-38
Abale a Yosefe apita kwao
26Ndipo anasenzetsa aburu ao tirigu wao nacokapo. 27Ndipo pamene wina wa iwo anamasula thumba lace kuti adyetse buru wace pacigono, anapeza ndalama zace; taonani, zinali kukamwa kwa thumba lace.28Ndipo iye anati kwa abale ace, Wandibwezera ine ndalama zanga, taonani, ziri kukamwa kwa thumba langa; ndipo mitima yao inawadera iwo, nanthunthumira, natembenukirana wina ndi mnzace kuti, Nciani ici Mulungu waticitira ife? 29Ndipo anadza kwa Yakobo atate wao ku dziko la Kanani, namfotokozera iye zonse zinaonekera kwa iwo;30kuti, Munthu mwini dziko, ananena ndi ife mwankharwe, natiyesa ife ozonda dziko.31Koma ife tinati kwa iye, Tiru anthu oona; sitiri ozonda; 32tiri abale khumi ndi awiri, ana a atate wathu; wina palibe, ndipo lero wamng'ono ali ndi atate wathu m'dziko la Kanani.33Ndipo munthuyo mwini dziko anati kwa ife, Momwemu ndidzadziwa kuti muli anthu oona; siyani mmodzi wa abale anu pamodzi ndi ine, tengani tirigu wa njala ya kwanu, mukani; 34idzani naye mphwanu kwa ine, ndipo ndidzadziwa kuti simuli ozonda koma anthu oona: comweco ndidzakubwezerani inu mbale wanu, ndipo mudzacita malonda m'dziko muno. 35Ndipo panali pamene analikukhuthula matumba ao, taonani, phukusi la ndalama la yense linali m'thumba lace; ndipo pamene iwo ndi atate ao anaona mapukusi a ndalama anaopa, 36Ndipo Yakobo atate wao anati kwa iwo, Munandilanda ine ana; Yosefe palibe, Simeoni palibe, ndipo mudzacotsa Benjamini: zonse zimene zandigwera. 37Ndipo Rubeni anati kwa atate wace, kuti, Muwaphe ana anga amuna awiri ndikapanda kumbweza iye kwa inu; mumpereke iye m'manja mwanga, ndipo ine ndidzambwezanso kwa inu.38Ndipo iye anati, Mwana wanga sadzatsikira ndi inu, cifukwa kuti mkuru wace wafa, ndipo watsala iye yekha; ngati coipa cikamgwera iye m'njira m'mene mupitamo, inu mudzatsitsira ndi cisoni imvi zanga kumanda.