05/04/2023
*ZODIAK ONLINE*
*"Hon. Zikhale Ng'oma, Maso onse alitu pa Inu,"- Nzika zokhudzidwa*
Gulu lotchedwa nzika zokhudzidwa zapempha nduna yoona za chitetezo cha mdziko kuti ichite zinthu mwachilungamo pa nkhani yokhudza kusamutsa nzika za maiko ena zomwe sizololedwa kukhala m'makwala kupita ku msasa wa Dzaleka.
Poyankhula kwa atolankhani mu mzinda wa Lilongwe, m'modzi mwa nzikazi a Wells Khama wati nduna zonse zomwe a Chakwera akhala akuzisankha mu undunawu zakhala zikubwera ndi nkhani ngati yomweyi koma palibe cholozeka chomwe chachitika.
Mwa ichi iwo ati nchifukwa nkhaniyi yalandilidwa ndi chikaiko.
Iwo ati akufunanso kudziwa kuti boma liwononga ndalama zochuluka motani pofuna kusamutsa anthu othawa mm'aiko awowa kupita ku Dzaleka.
Kumbali Ina nzikazi zayamikiraso mkulu wa polisi a Merlyn Yolamu kaamba komanga anthu omwe akuganizilidwa kuti adapha mkulu wina wochita malonda mu mzinda wa Lilongwe a Emmillie Halimana Noel chaka chatha.
Iwo ati alondoloza nkhaniyi mpaka ayiwone pomwe ithere.
*☄️[email protected]*