27/05/2026
LERO TIGAWANEKO ZOKHUDZA GASTRITIS (matenda okhudza Gas)
Awa ndimatenda omwe amawonongo nkati mwa mimba maka layer yomaliza .
KODI CHIMAPANGITSA MATENDAWA NDICHAN 🤔
1 munthu wina aliyense mimba mwake muli diffensive mechanism imene imateteza ku nkati mwa mimba musaonongeke, chifukwa cha acid defensive mechanism iyi imatha kuonongeka then matendawa amayamba.
2 acid komanso ma enzyme ena , muthupi amagwila ntchito yogaya zakudya .nde acid amene yu komanso ma enzyme akakhala k*t ndiwambili amalowa nkati mwa mimba ndikupangitsa inflammation then munthu amayamba kudwala. Apa kwenikweni pokhudza ACID KOMAXO ENZYMES PANVEKE NDITHJ! KUGAYA kwazakudya zimatheka kamba kazinthu ziwirizi.
3 kukhala ndi nkhawa ,izi zimapangitsa k*t uthenga utumuzidwe ku brain later pamapangidwa acid wambiri then kuyamba kudwala matendawa.
ZINTHU ZINA ZOMWE ZIMAYAMBITSA MATENDAWA.
"Ma infections eg H. Pyrolus."
"Mankhwala ena ochosa ululu ngat aspirin komanso bufen".
"Kumwa mowa komanso kusuta ". Akachasu ndi anzake
"Zakudya za poison ".
ZIZINDIKILO ZA MATENDA WA.
✓m'mimba kumangonva kupweteka komanso k*tentha.
✓kunva nselu mwinanso kusanza.
✓ kumangonva ngat wakhuta kale.
✓ kusanva njala.
✓kumanva ngat zinthu zikubwelela kuchoka M'mimba,nd zina zambiri. Kuphwisaphwisa, kulira kwammimba, kuchepa kwachilakolako cha chakudya.
KAPEWEDWE KA MATENDAWA.
=Pewan kusuta komanso kumwa mowa
= Pewan kudya zakudya Zama spicy komanso nyemba
= Masewelo olimbisa thupi pangan
=Chepesan nkhawa