Calvin top 10 love stories

Calvin top 10 love stories Kuwelenga ngati mukuwonela

😭😭😭😭😭😭😭😭😭 MWINA OLAKWA NDINE😭😭😭😭Part one Story written by calvinLike Calvin top 10 love storiesWow congratulations mwayi...
13/09/2025

😭😭😭😭😭😭😭😭😭 MWINA OLAKWA NDINE😭😭😭😭
Part one

Story written by calvin

Like Calvin top 10 love stories

Wow congratulations mwayi wandibelekela mwana amene ndimafuna ndipo ukangotuluka kuchipatala kunoku uwona kuti ndimatani ase

"Mmmmm mwakondwatu kwambili Bambo tangomusani dzina basi mungakonde azitchulidwa ndi dzina lanji?"

Palibe Zina Lina loposa junior ndipo ameneyu nde mbewu ya dzina langa ndipo dzina langa silizafa chifukwa Cha mwana ameneyu

Uku kunali kuyankhulana kwa bambo ndi mayi mofolo pa tsiku limene mayi mofolo anabeleka mwana wawo woyamba wa mmuna koma anali atabeleka kale mwana wankazi woyamba dzina lake Alice

Zinthu zinali kumbali ya banjali ndipo kunali chisangalalo kuti tsopana apeza mwana amene bambo a apanyumbapa amamufuna ndithu moti anapanga chilichonse chimene akatha kuti awawonetse akazi awo kukondwa kwawo

Ndipo tsiku lachiwili mayi kuchipatala anawatulitsa kuti apite kunyumba kunali chisangalalo bambo a ju atayitana anzawo kuti Ali ndi phwando chifukwa chakubadwa kwa juuuu ndipo kunali kudya ndi kumwa chifukwa chobadwa kwa juuu mwana yekhayo okondedwa ndi bambo apanyumbayi

"Komatu bambo mwNdidabwitaa Alice nabadwa koma simunasangalale ngati mmene mwasangalalila lelo"

"Kodi make simukunvetsa pati mwanayutu ndi wanga woyamba wammuna ndisiyen ndinjoye ine mwana yekhayo amene adzasunge dzina langa"

"Ayi zikomo chifukwa chondilemekeza bambo ndiku ndikusangalala kuti ndakubweletselani chimene mumafuna mothandizidwa ndi Mulungu"

Ukutu kunali kucheza kwaayi ndi bambo Ake a juu mayi atadabwa ndi mmene anasangalalila bambo a juuu

Masiku anali kutipa ndili juuu anali kusotsa nsinkhu ndi mawonekedwa kamba ka chikondi chimwe banjali amamuwonetsela

Masiku anali kupanga ma week ndipo nawo ma week sanainve nawo anali kupanga miyezi ndipo miyezi sinachepele Kaba nayo inali kupanga zaka ndipo tsopano juuu anali Ali ndi zaka 5 zakubadwa

Ndipo makoli a juuu anali kupeleka malangizo kwa anawo awiliwo kuti azipitiliza kukula ndi makhalidwe abwino

Ndipo ngati makolo anayesesa mmene angatheke kuti anawa akule ndi maganizo abwino

"Mukunama mwana wanga sangapange zimene munenazo Kodi basi kukhala ndi mwana wang'ono ngati ameneyu waulemu wake nde kuti basi mukufuna muzimupezelela mwana wanga sangapange zimene mukunenazo mwanva"

To be continued

09/09/2024

The choosen king part 1

13/08/2024
30/07/2024

🤣🤣🤣FOOL OF SCANDAL PART 2🤣🤣🤣

Story written by Calvin

Like calvin top 10 Love stories

Tinalekesa Heinz ndi brother wake mada akupita ku holiday Kwa aunt awo

"Takulandini anyamata nkhalani omasuka kuno"

Anawalandila aunt awo omwe tizingowatchula kuti aunt vic

"Kodi aunt mmmm please tisamangokhalila ku mpanda Kodi simungatilole kupitako paja tikaponde ponde"

"Aaah zimenezo nzochita kufusa? M***a kupita palibe vuto"

"Aaah ine nde sindipita ndizisewelaba game yomweyi pita wekha"

Anayankhula Heinz uku akusewela game ya FIFA

Sanankhumudwe mada ayi ndipo anatuluka pa geti uku kolowela asakukudziwa akuti kuzungulila kumayadi kuti akuwone bwino bwino

"Inu tandipaseni chikwama changa mwanva ndakuyambani?"

Ananva mawu chapatali ndi ndiposo chapasogolo mada ndipo mawuwo anali a nkazi ndipo anapita akawone kuti pakuchitika chani

"Kodi mumalimbana Ndi ine bwanji mesa ndimakuuzani kuti sindifuna kumacheza nanu ine"

Panali anyamata atatu ndipo amaponyelana chikwama Cha tsikana opanda dzinayo ndipo kunena monenetsa kantsikanako kanali Kokongola kwambili ndipo kantima kanagunda ndipo kanali katazikonzekeletsa zokathandiza nkaziyu

"Eeeeh Kodi pakuchitika chani apa tamubwezeleni nkazi wa ine chikwamacho"

Anthu anadabwa ndimawu amene mada anayankhula ndiposo nkaziyo anali odabwa kunva kuti munthu amene sanayambe atamuwonako akumutchila kuti nkazi wake koma pofuna kuti athandizidwe analolela kukhaladi bwezi lake Kwa nthawi imeneyi

"Eeeeeyaaa iwe ndi amene ukumapangitsa kuti nkaziyu azitiyankha mwano eti? Lelo nde uziwona "

Anayankhula moopseza nyamata mmodzi mwa anyamatawo uku akulowela komwe kunali mada

"Mmmm mwabwela mwa phumatu kwambili Bea tabwela kuno"

Anamukodola ntsikana opanda dzinayo ndipo anapitadi kukakhala kumbuyo Kwa mada uja
Ankulu uja anapsa ndima ndipo anathama kuti akamenye mada koma mwatsoka akufika mada anaponya kick ndipo linafikila mmimba mwa kamuna uja ndipo anagwa pasi uku akubuula ndi ululu ndipo sanakwanitseso kudzuka

"Musamudikilile kuti adzuka uyu ndathana naye kale wina atha kubwelaso ndimuwonetse zimene ndamupanga nzanuyi"

Anzake a nkuluyi anangomuponyela mada chikwama chija ndikumudzutsa nzakeyo nkumawona nsana wa njila

"Zikomo kwambili wandithandiza"

Anayamba ndikuthokoza nkazi opanda dzina uja

"Ndangoyenela kutelo Kwa nkazi okongola kwambili"

"Mmmm sine okongola ayi koma dzina lako ndi ndani"?

"Ndine mada nanga iweyo ndi ndani?"

"Ine ndi faith"

"Ndathokoza kukumana nawe faith"

"Ineso ndokoza ponditeteza Kwa anyamata aja, basi ndizipita"

"Mmmm nthawi yomweyi? Anyamata aja sanapite patalitu atakuwona uli wekha wekha antha kukupanga chipongwe tiye ndikakusiye kwanu"

Pochitadi mantha faith anavimela kukamusiya kunyumba kwawo ndipo mmene amachezela zinachita kukhala ngati anachezako ndipo izi zimachitika kuti awone kufulumila kufika ku nyumba Kwa faith

"Basi ndi zipita ukafika kwanu undiyimbila"

Anayankhula faith uku akulowa mu mpanda mwakawo chifukwa pa nthawiyi anali anapasana kale ma phone number

Nkhan ikupitilila

🤣🤣🤣🤣FOOL OF SCANDAL part 1🤣🤣🤣Story written by CalvinLike calvin top 10 Love stories  "Yaaa  anthu aja vuto nclass muja a...
29/07/2024

🤣🤣🤣🤣FOOL OF SCANDAL part 1🤣🤣🤣

Story written by Calvin

Like calvin top 10 Love stories


"Yaaa anthu aja vuto nclass muja amawona ngati ifeso ndi mbuli"

"Nde zachita bwinotu mmene ntatsekelamu zachita kuwonetselatu kuti ife ndimizyanya ase nanga tiziti Pali amene wakhoza kuposa ife"

"Mayazi sunanve anachita kuti pa sukulu pano ana amene ankhoza bwino ndi awili okhawa basi komaso tikanankhala kuti Pali amene watiposa tikawona akumupasako mphatso ngati zimene talandila ifezi kaya"

"Eeeh eee ana inu mukungozilankhula nokha nokha bwanji? Tizisimumandiwona kuti ndaima kale kale pano?"

"Aaah amayi kumanena kuti mwabwela muzapezeka mwatinva tikukujedanitu, komaso kuchipanda Kwa anyamata samangolowa usanagogode simuzawona zodabwitsa?"

"Aaaah inu a hestings chodabwitsa chake chani mukunena inucho? Nyumba yanga yomwe ndizikhala momangika ngati mwakula samukani"

Anayankhula moseleula mayi Kwa ana ake awili omwe anali amapasa komaso ana okhawo apabanjapa

Kungofotokoza pa nkhano za banjala. Banjali ndila mayi ndi bambo dzimbili ndipo makolowa anali ochitika ndithu mwa size yawo chifukwa onse awili anali pa ntchito za bwino kwambili ndipo pankhomo pawo panali pa mwana alilenji.
Anyamata mmene amakambilana zakusukula anali Ali form 3 ndipo pa tsikuli anali atangoweluka kumene kusukula komwe amatsekela ndipo anali ana anzele kwambili pa sukulu ponse ndipo panthawiyi nkuti atakhoza bwino kwambili kuposa ana wose apasukuluyi

"hestings mukapuma pang'ono ndi madalitso mundipeze pa balaza ndikutumeni"

Anamali choncho mayi a anawa akutuluka kuchipundachi

"Chabwino amayi"

Anayankhila pamodzi ngati kuti anachita chopangana

Sipanatenge nthawi ana aja anapitadi pa balaza panali mayi awo ndipo anawatuma ku nsika kuti akagule zina ndi zina

"Eeeeheee kusukulu kuja kumaziwonetsa madolo pamene paja chifukwa mwankhoza ma number one nonse? Ndimawona ngati sitikumanasotu ma phwanga"

Anayankhula nyamata wina Kwa ana amapasawo

"Aaaah man gift bwanji Kodi mwabwela ndi phumatu amafikila choncho mukanadekhatu komaso mesa inu mumadzithemba kuti apa geli paja wanzelu ndinu tinangofuna kuti tikuwonetseni kuti ifeso anatilenga ndi ubongo wa anthu 6"

Anayankhila hestings chifukwa iye anali munthu osaugwila ntima kusiyana ndi chimwene wake madalitso

"Usandiyankhule mopusa ndikuputha wanva sindinyengelela paja ine kaya mukuzinvala ndalama kaya chani ine zopusa sindipanga nawo"

Anayankhula moopseza gibo uku akumukakha hestings mwa mphavu kwambili

"Aaah guys zisafike pamenepo ayi nkhani yake ndi iti yoti muzimenyelana panepo man gibo tamavaya tikambilana nthawi ina iweso henz tiyeni tizipita"

Anayankhula motheza nkhani madalatso ndipo Kwa iye amafuna kuti pasachitike ma phokoso aliwonse pa nsewupo
Koma zomwezi analakhula madazi sizinamunvekele bwino gibo chifukwa chilinga chake chinali chisanakwanilotsidwe Kwa anyamata awiliwa ndipo chifukwa Cha nkwiyo gibo anapeleka mbama Kwa mada.

"Nde ukumumenyelanji m'bale wanga?"

Anafusa funso henz Kwa gibo ndipo fusolo limasagana ndi bakela la mphavu lomwe linadza mozizimutsa Ku nkhope ya henz

Gibo posawonetsa kufuoka anaponyaso bakela lake Kwa henz ndipo kunena chilungamo henz amachepela Kwa gibo chifukwa gibo anali wa mphavu kutengela ndi henz, madalitso anayesesa kulelentsa anthuwo koma ayi ndithu anyamata analimbilana mitima awa zinachita kutengela gulu la anthu omwe ankadutsa pa nsewupo kuti awaleletse .

"Uli ndi mwayi akuleletsa koma dziwa kuti ndewu imeneyi sinathe ase ndipo kulikonse ndizikupezaniko ndizikuthibulani ma phwanga"

Anayankhula choncho gibo akukokedwa ndi anthu oleletsawonkuti asiyane ndi anyamata amamenyana nawowa

Mada ndi henz anatolela tizinthu tawonanawatuma tija nkumabwelela wakwawo ndipo munjila samayankhula mpaka anakafika kwawo ndipo makola sanachite kufusako kuti kunsewu kumachitika chani maka Poona ndi mmene nkhope ya hestings imawonekela pa nthawiyi chifukwa inali itatupa ndithu

"Mwayamba ndewu sichoncho? Mumamenyana ndi ndani mpaka kukutupitsa choncho?"

Anafusa mayi

"Amayi ingozitayani zimenezo"

Anayankha henz akusutha kupita kuchipinda kwake ndipo mada naye anamutsatila ndipo atalowa kuchipinda chawochi anatseka chitseko kuzitsekela nkati

"Kodi akuwona ngati awina amene aja ndewusi sinatha ndipo tikabweza ndipo chikhulupilila choti ndewuyo tawina kale tili nawo"

Anayankhula mozilimbitsa ntima henz

Mada anakatenga galasi ndikumawonetsa nkhope ya henz mawu ake Ali nkamwa ndipo onse anayamba kuseka ndi mmene Heinz amawonekela

"🤣🤣🤣🤣 Eeeeh koma man anthu amamenya amwene wakulu ngati inu nkhope kuti pa choncho"

"🤣🤣🤣 Zoti yafika apa ngatiso ndimadziwa? Ukutathauza kuti kunsika konsekuja ndayenda nkhopeyi Ili chonchi? Vutoso ndi iweyo ase mada ine ndimateteza iweyo iwe koma or kundithanzila inuyo man ndinu opoyila man kaya ndukufatsa kaya ndi chani koma simungafananebe ndi yesutu"

Anachexa anyamatawo ndipo chifukwa chochedzstsa anayiwalaso kuti kumasanaku kunachitika chani mpaka pamene Bambi awo anabwele kuweluka ku ntchito

Chakudya chama dzulo chinakonzedwa ndipo anadya banja lonse mwanthawi zonse

"Ndanva zonse zomwe mwapanga kumasanaku ndipo ndisanzanve kuti mwapangaso nyasi zimenezo ndipo pachifukwa chazimenezi ndikupititsanu Kwa aunt anu mukhale kumeneko mpaka tsiku lotsegulila"

Anayankhula mokwiya ndiso mowonetsa kusasitha maganizo pa nkhani yoti anawa apite Kwa achemwali awo ndipo kumbali ya anawo nawo anasangalala nchifukwa Kwa aunt awo nde amasangalalakoso kwambili

Nkhani ikupitilila

11/03/2024

🩵👺🩵👺🩵👺 JENNIFER PART 13🩵👺🩵👺🩵👺

Story written by Calvin

Like Calvin top 10 love stories on Facebook

Weekend inafika mongadi mwa mwambo anatengana anthu okondanawo kuti apite kokayenda

"Honey ndisaname sindinkayembekezela kuti ungandilole ase ndipo nsakubisila ndizapanga chilichose chothekela kuti uzisangalala"

Anayamba kuyankhula ti nkhani ta chikondi William tomukopa Jennifer

"Ndipo ndisakubisile Jennifer I hope Mulungu tsiku lija ankapuma lija Anali akupanga iwe ase ase chifukwa nde anakufasililatu"

"🤣🤣🤣🤣 Usandisekese wanva komaso iweyo ndi wowoneka bwinotu William moti kukulola iweyo ndinangoyenelela basi"

"Mmm koma Jennifer, *So far, every moment we've spent together has been awesome. But I promise you, that the best is yet to come.*"

"Chilungamo? Honey ukudziwa kuti *Somehow just hearing your name gives me butterflies.*

"Ndinkani ndikuti ndimakukonda kwambili ndipo *I can't decide if the best part of my day is waking up next to you, or going to sleep with you. Hurry home so I can compare the two again.*"

"Mmm koma William *Thank you for always making me feel like the most beautiful woman in the world 💅💄👑👄*

Chifukwa Cha machezedwewa sanachedwe kufika komwe anthu awiliwa amapita ndipo anapeza Malo abwino ndiposo okomwela anthu akondana ndipo anakhala pasi nkumacheza

"Jeni Kodi ufuna kudya chan?"

"Aaa William Nena iweyo ine ndudya chimene utadye iwecho"

"Ase tangotubweletsela chips and chicken ndi mabotola a coco awili"

"Aaah ine coca-cola sandisangalatsa ulibe red wine🍷"

"Aaa pepan aunt tilibe chakumwa chimenecho"

"Okay chabwino nde ungondipasa madzi"

Anapeleka madzi ndipo onse anayamba kudya uku akumacheza

Kunali kucheza zakoma zija ndipo Jennifer mapaka anayamba kuiwala zomwe anapitila kumaloku ndipo atacheza kwakanthawi ananva china chake ngati chikumuyenda ndipo ankati kati ananva mawu a Melissa

"Jen wakomedwatu panga zothekelazo ife takonzeka kale kuno utipeza loom 7 ndiyomwe uzalowe"

"Jennifer Jennifer"

William anamugwenyeza Jennifer maka atawona mmene chibwezi chakechi chinakawonekela pa nthawiyo coz or kumuyankhula chotani samanva

"Yes William ukuyankhula"

Amazizimuka Jeni chifukwa chogwenyezedwa ndi William

"Bwanji uli bwino bwino koma Jennifer "

"Yaaa ndili bwino bwino William kungoti ndatopa Kodi sitingapezeko loom pa Malo p***a nkukapumako"

"Aaah ndikuwona ngati kuti tizingopita bwanji coz ukuwonekadi kuti watopatu"

"Aaa William tatiye ndikangogonako wezi sindikufuna ntakutalikila ayi"

"Ukudziwa chani Jen kumenekotu nkwa anthu awili nde titha kukapanga zolakwika nde bwanji kupewa zimenezo tizingopita?"

"Aaaa iwe ase nde or titakapanga ndikakhala ndikupanga ndi munthu olakwika mesa ndikupanga ndi amuna anga to be"

"Yaa ndichoncho koma lelo ine sindinakonzeke tiye tizingopita"

Anapeleka ndalama imene anagwilitsa ntchito kwa oyang'anila mwalowa

"Aaaa William ndalama ndilipila usalipile ayi"

"Wachedwa Jen ndalipila kale"

"Ine ndalama ndili nazo zambili and sindinayambeko ndadya ndalama za mamuna ine"

"Lelo wayamba eti bwanji mmene zimakomelamo uli ndi ine honey ndipo moyo wako ndiuvetsa kukoma "

Mosanyinyilika ngakhale sizimamusangalatsa anakakwela galimoto ya William ndikumabwelela kwawo

"Koma kweni kweni chimene wakanila ndi chani kuti tikagoneko ku loom "

*Mmmm Jeni ndumakusungila ulemu ine ndipo sichanzelu kuti tikakhale nawo amodzi chibwezi chitintangapanga mwezi imodzi onkha"

"Ineti sindimafuna kuti tikagonan ayi ndumangofuka kukapumula basi "

"Nde usadandaule paja kunyumba ndimakhala ndekha nde titha kupita imagine wezi"

Asanayankhe Jen ananva mawu a Melisa kuti pita kunyumba kwakeko, ndipo izi zinamutsimikizila kuti Melisa Anali nawoso pa ulendowu. Chipangizo choyenda pansichi chinalowa ku mphanda kwa William ndipo atalowa nyumba Jennifer anagona pa mpando ndipo chifukwa Cha tulo William anamunyamula ndikukamugoneka ku chipinda chake
Ndipo mmene amanyamulidwa Jeni amanva koma amachita dala kuti William akamupanilile kuchipinda chomwecho

Koma mmene amamugoneka pa bed la William Jennifer anagona tulo tofa NATO

Nkhani ikupitilila

10/03/2024

🩵👺🩵👺🩵👺 JENNIFER PART 12👺🩵👺🩵👺🩵

story written by Calvin

Like Calvin top 10 love stories

Game inayambiks ndipo amachita kuthandizana ndi Melissa uku akumupopa zoyenela kupomapazo ndipo a head zoti anthuwa alipo awili samadziwa nkomwe mmene round yachiwili imatha kuti ahead alibiletu ndi mphavu nkomwe

"Eeeh Jennifer iwe ndi nkhani zina eeeh simmene ndilili apapa umatha bwanji sindinagonaneko ndi mwana wasukulu ndikundipanga zimene wandipangazi umatha kwambili"

Anayamikila a headmaster pokonda zimene Jane anawapangila

"Koma nde ndatopa bwanji ndikunvaso chizungulile tapita ukandigulile kaye drinking panjapo"

" Mmm dear tamangotiyeni tizipita pajatu ndatuluka anthu asakudziwa"

"Oooh ya chabwino basi tiye tizipita koma nde eko 10,000 iyi uwone chogulila munsikamu"

"Aaah ayi dear uzandipasa nthawi Ina ine ndalama ndili nazo nzokwanila ingogulani mafuta basi"

Ahead Anali kusangalala kuti apeza nkazi osakonda ndalama komaso odziwa kupeta ndipo amachita kudziwa kuti akafuna abuja aazidya koma osalipili

Anatuluka ku ndikukakwela galimoto yawo ndipo atafika mu nsika Jennifer anawawuza kuti azipita basi akawonana mu compus ndipo zinathekadi

Ali njila kuyendetsa galimoto yawo chizungulile chimachiuka chuluka ndiposo Anali ofooka kwambili ndipo anayesa kugula energy drink kuti mwina abwelelamo koma ayi ndithu zimangochulukila chulukila ndipo anaganiza zodzela ku chipatala .

Atafika kuja anafika Ali ofooka kwambili ndipo atawagoneka anawapeza kuti magazi awo anthelatu. China chake chinawabwelela ahead tsopano kuti Jane Si nkazi wamba ndi nkani wakana ndalama kchufukwa zimene amafuna kuti atenge zatheka. Anapanga pa dongolo a zamagazi koma mmene adokotala amabwela kuti awapase magazi anapeza kuti bambowa amwalila ndipo chimene chinawapha abambowa ndikusowa kwa magazi nthupi

Masiku Anali kupita ndipo masiku anapanga ma week ndipo nawo ma week Anapanga miyezi imene inapanga zaka ndipo tsopano Jen analemba mayeso ake a form 4. Chifukwa Cha nzelu zimene mwanayi Anali n**i anakhoza bwino mayeso ake ndipo anamuyankhila Kuma university apamwamba amene ana nkhoza bwino amapita ku university nde nyanyi analimbikitsa achinyamata anzake kuchita zinthu zomwe iye amapezapi phindu ndipo anali kuphuzinsa anthuwa ambili zakumidima ndipo izi zimapangitsa kuti ku gulu lake kuja anthu azimukondaso kwambili ndipo anali kupanga chilichose chothekela kutapitilizebe kupeza ulemelelo pa dziko lapasi

"Kodi sister tayimani kaye ndimangokuwonani mukamadutsa apa Kodi mumaphuzila kuti"

"Bwanji kweni kweni iwe ndi ndani npaka kufuna kudziwa za ine ?"

"Popeza wanfusa ndikuyankhabe ine ndi William ndipo ndimakhala mmudzi mommuno, ndisaname your the beautiful girl I av never seen"

"AAA iwe usandinyase wanva"

Ananyamuka nkumapita Jennifer ndipo anakafika kwa nzake kapena kwa nkholo lake Melissa

"Melisa ndipo zimene ndaziwona ine zodabwitsa bwanji "

"Bwanjiso Jennifer iweyo kuwona zodabwitsa? Chachitika ndi chan "

"Iwe eti nyamata wina wake wandifusila eti?"

"Nde chodabwitsa chimenecho wafusilidwa ndi angati iwe pofika nsikhu umenewo usandisekese wanva?"

"Mmm koma nyamata ameneyo nde wangondidabwutsa kaya bwanji kaya"

"Panga zoti tipindulemi mmenemo yathu ija ndipo uyo nde ndikatengamo zambili"

"Dikila tipange zomwezo waishosha ekha ameneyo"

Anagwilizana zoti apheso William pofuna kusangalatsa anzawo akumidima ndipo pamene anafika Jen panali pakuti akatsimikiz kuti uyu afe aphadi ndipo ndizimene anagwilizana kuti apange pa William

Tsiku Lina anachita kukadutsila Dala kumene William amakhala ndipo William anamuwonadi nkazuyit

"Hey fine girl tandidikile wezi"

Anayenda ngati sakufuna ndipo William anamuthamangila nkaziyi

"Mami bwanji Kodi mesa timakuyitanani"

"Iwe inetu zopusa ayi asewanva"

"Komabe Kodi dzina lako ndi ndani"

"Ndine Jennifer bwanji"

"Wow dzina lofanana ndi khope Yako ase ndiwe okongola bwanji ndimakondatu kukuwona ukudutsa apa Kodi umaphuzila university Ili apoyo?"

"Ya ndikumene ndimaphuzila"

"Ndisakunamize janepher pakanankhala kuti pa school apopo palibe iweyo bwezi university yonseyo palibe nkazi okongola "

""Choka iwe wanva🤣🤣🤣🤣 "

Osanama William anacheza naye momasuka kwambili ndipo Jane Anali asanachezetsedweko choncho ayi ndipo anakopeka ndi William koma cholinga chake chinali chithana ndi william.ndipo William mosadziwa kanthu anaponya mbalume William ndipo Jennifer anavomela uku akudziwa kuti mbuzi yagwela kale mumatchela

Panadutsa ma week atatu anthuwa Ali pa chibwezi ndipo tsiku Lina William anamupepha kuti akadyeko Malo odyela ntown ndipo Jennifer analoladi

*Melisa William wazigwetsela yekha akuti weekend tivaye out"

"Yes ndizimene ndimadikilila nsaname ameneyo nde sindinkansiya or kadothotu"

"Mutaye eneyo Ali ndi ife"

Week end inafika ndipo mongadi mwa mwambo anatengana anthu okondanawo kuti apite kokayenda

Tabwelani pa Whatsapp kuti story izikufikani mosavuta anzanu akulo group ndi 500 kwacha yokha kwa amene akufuna 0993222379 ndiyo number yanga

Nkhani ikupitilila

👺🩵👺🩵👺🩵 JANEPHER part 11🩵👺🩵👺🩵Story written by CalvinLike Calvin top 10 love stories"Koma nde tiye ukansanzike kwa akulu a...
29/02/2024

👺🩵👺🩵👺🩵 JANEPHER part 11🩵👺🩵👺🩵

Story written by Calvin

Like Calvin top 10 love stories

"Koma nde tiye ukansanzike kwa akulu akulu"

Anatengana kupitisana ku gulu lawo lija ndipo atafitokoza nkhaniyi anthu anawombela mmanja ndipo amavomeleza kuti apa akanakhala ndi mpata wambili obweletse nsembe ku gulu lawoli

Ndipo poonetsa kukondwa ndinkhaniyi anamuchuna wezi wezi ndipo mmene amatuluka kumaloku nkuti Jen akuwoneka okongola kwambili kuposa chobadwidwe chake.

Mammawa watsikulo ananyamuna kukayamba sukulu ndipo atafika anapezadi Malo ndipo ngakhale anasiyila STD 7 koma tsopano kamba koti Anali ndi zaka zambili tsopano anayambila form one

Ngankhale Anali form one koma sizimawoneka kuti analekeza std 7 koma mwana Anali ndi nzelu zachibadwidwe chifukwa ndi amankhoza osati masewela ayi

"Jennifer I want your ku office kwanga ukaweluka"

Anayankhula a head akutuluka mu class ya achina Jennifer. Ataweluka Jennifer anayenda straight ku office ya a headmaster ndipo anawapeza akumudikilila

"Ndakupezani ahead paja mumandifuna?"

"Yaaa ndizoona Pali nkhani yoti tikambilane, koma ineyo Jen sindinawoneko nkazi wooneka bwino ndiso okongola ngati iwe, nde ndimawona ngati kuti titati tanvana utha kukhala ndi mwayi oti zinthu zizikuyendela pasukulu pano"

"Mukutandauza chani a headmaster pamenepa tamasukani"

"Iweyo ndi ine tizinvana nzimene ndikutathauza ndipo ndiwe wankulu ukudziwa zimene ndikunena,"

Apa Jane anayitulukila ndipo anavomela kukhala chibwezi Cha a head ndipo kwa iye ankangoti eya! Yagwelamo yekha ndipo mayesesa kuti ahediwa azimukinda kwambili

"Jennifer weekend ndikakupeze mu nsika wapafupi ndikunowu tikavaye pena pake "

"Okay chabwino ndizikakudikilani"

Anayankha mofupikitsa nkhani Jane ndipo tsikuli litafika anapita kukayimba pamene anagwilizana

"Hello Melissa bwanji zabwino ahed ayipepha inkha nde tabwela tizathandizane"

"Kuli chani kumebeko nde tikamumalizatu okay ndupezani takamuyambe"

Atangofika a ahedi anamutenga ndikupitana kaye pa rest house yomwe inali yoyandikana ndi nsikawon

Ndipo mmene anatsegula room anamupeza Melissa Ali bulanda ngati kuti amadziwa kumene anthu awiliwa akakumane koma chopasa chidwi chinali chakuti anamuwona ndi Jen ekha ndipo a head samawona kalikose

Game inayambika ndipo amachita kuthandizana Melisa ndi Jen uku akumupopa .........

Akulu akulu ndusinza ndimaliza mawa

👹👹👹👹 JENNIFER PART 10👺👺👺👺STORY WRITTEN BY CALVINLIKE CALVIN TOP 10 LOVE STORIES"Hello mwasowatu aunt, zikutheka koma"Izi...
28/02/2024

👹👹👹👹 JENNIFER PART 10👺👺👺👺

STORY WRITTEN BY CALVIN

LIKE CALVIN TOP 10 LOVE STORIES

"Hello mwasowatu aunt, zikutheka koma"

Izitu zinawabalalisa makolo onse amene Anali nyumbamu ndipo an**indikila kuti apa sipatha bwino basi

"Chonde Jennifer please ukufunaso Chan? Tisiye chonde unatichotsela chisangalalo chinthu potiphela mwana wanga nde ukufunaso chani"

"Ndinakuphelani ndi ine mesa munadya nokha mwana wanu inu"

Anayankhula mwa mwano ndipo izi zinakumbutsa aunt mawu amene amakonda kumuyankhula Jennifer pamene anakhala naye limodzi

"Chonde Jennifer ndikudziwa ndinkakuyankhula mosakhala bwino koma chonde peza mpata mu ntima mwakomo undinkhululukile"

Ngakhale amayankhula koma makolowa Anali asakumuuona Jennifer akungonveka mawu okha

"Mwachedwatu aunt komaso Inu madala mukukumbukila munandiuza kuti mumafuna mutandigona lelo nde ndabwela mupange zimene mumafuna"

Ayi usapange zimenezo ndinkangoyankhula ndimakudziwa chimene ndikupanga nde chonde pita utikhululukile please "

"Komatu mwachedwa kwambi koma ndakunvani ndipanga zimene mwanena ndapita"

Chitseko chinanveka kutsekulidwa ndipo chinavekaso kutseka zomwe zinasonyeza kuti Jen wapitadi

Bambo apatu amene uja sikuti watisiya iyayi chofunika ndikuyamba kupephela molimba kuti asatiwonetse zowawa pakhomo pano"

"Yaaa komaso mwina tingosamuka tikayambe kukhala pa rent"

Anagwilizana zosamuka mawa kukangocha ndipo akakhale kutali kuti jen asakwanitse kuwapeza

Mmene mmawa kumacha aunt a Jennifer anadzuka kukagwila ntchito za pankhomo ndipo anapita kukasiya madzi osamba ku bafa kuti Amina awo asambe koma pokawadzutsa anadabwa munthu sakuyankha anayesa kuwagunyuza koma munthu Anali gwaaaaa atawumilatu ndipo apa ndipamene Anadziwa kuti bambowa amwalila.anakuwa akulila aunt a jen ndipo anthu atanva kulilako anathamangilako kuti akawone chimene chimachitika ndipo kwa aunt inali infa yowawa kwambili maka kulu anthu awili kuphatikizapo amuna awo womwe amawadalila pa chisamalilo chawo chonse.

Ndipo anthu amene Anali pa fupi ndi mayiwa ananva chisoni kwambili ndipo inali infa yowawa ya munthu oti Anali asanadwaleko

"Janepher zakhala bwanji kuitanisa meeting yodzidzimutsa chonchi"

"Ulemu wanu anthu Inu ndipo ine chifukwa chokuitanani ndimafuna ndipeleke nsembe imene ndili nayo"

"Nsembe ? Ifetu sitinakutume nsembe iliyose kuno"

"Yaa I know ndinkani ndafuna ikhale surprise kwa Inu mfumu, pofuna nanu mundipangile zinthu za bwino ngati zimene mumandipangila kale"

Anamuthokoza Jeni chifukwa chifuna kukulitsa mphavu za kumidima zomwe Anali kukhala ndi kupeza ulemelelo wakewo

"Koma tikukuthokoza chifukwa chakulimbikila kwako Jennifer koma apa wapeleka nsembe anthu awili ochokela banja limodzi ndipo chifukwa Cha ichi sukuyenekaso kuzapeleka nsembe kuchokela ku banja lomweli ndipo apa basi pazafunikila anthu Kwina osati banja lomweli"

Zinamuyipila Jen chifukwa Anali asanathane ndi aunt ake ndipo nanga akanatani munthu anangozisiya

Masiku Anali kupita ndipo anayamba ma mission osiyana siyana ncholinga Choti azikulitsabe ulemelelo wake pa chuma chake ndipo anali kuchitsa ngozi ndipo anali kugona ndi amuna osiyana siyana ncholinga chowatenga zijazi. Mukuziziwa Inu sindingachite kukuuzani

"Melissa nsaname ndimakufuna ndimafuna undithandize zinazake"

"Tanena Jen ndili pano chifukwa Cha iwe"
Munthune ndimafuna ndinayamba school koma ndikufuna iweyo undithandize ngati nkholo"

"Palibe chovuta ndipo waganiza bwino bwanji Si kumeneko uzikapangaso sopindulila gulu lathuli"

"Ndipo usakayike ndichimene ndupitila"

"Zili bwino nde ukonzeke mawa ndikakulembetsele"

Tikunena pano anzanu amaliza story pa Whatsapp kwa amene akufuna kuyamba nawo ya untill death bwelani pa Whatsapp ndipo mundipeza pa 0993222379

Nkhani ikupitilila

👺👺👺👺JENNIFER PART 9👹👹👹👹👹Story written by CalvinLike Calvin top 10 love storiesZinthu sizinavekele bwino aunt ndi amuna a...
28/02/2024

👺👺👺👺JENNIFER PART 9👹👹👹👹👹

Story written by Calvin

Like Calvin top 10 love stories

Zinthu sizinavekele bwino aunt ndi amuna awo ndizo zomwe anawayankha ku police koma anthu a mmudzi analonjeza zomusaka Jeni kuti nawo angophelatu koma nanga zikanatheka bwanji munthu wina aliyese samadziwa komwe Jeni amakhala

"Zikomo chifukwa chokwanilitsa zimene tinalonjezana jeni ndipo apa wawilikiza kawili ulemelelo wako wapadziko lapasi"

"Ndizapanga chilichose kufuna kulemekeza Inu mfumu"

"Ndinthawi yoti ukhale ndi galimoto Yako Yako tsopano"

"Zikomo mfumu koma ine sindingakwanitse zaka 18 zakubadwa ndipo sindingaloledwe kuyenda galimoto"

"Jennifer usamayiwale ife ndiye aniwake a ulemelelo wakudziko palibe chimene chingatilephele"

Anayankhulana kumuuza zina ndi zina zokhuza galimotoyi ndipo atavomeleza anamubweletsela bokosi ndipo anagona mmenemo

Ali nkatimo chomwe amanva ndi nyimbo ngakhale samadziwa kuti nyimbozi nzachiyankhulo chanji ndipo kamba kokhala ekha mudima wa bokosilo anagona tulo ndipo mmene amazizimuka nkuti Ali mu galimoto yopuma ya Toyota mack x

"Jane galimoto wakwelayi ndi ulemelelo wako oyamba wapadziko lapasi ndipo dziwa izi bokosi unagonamo ija ndi galimotoyi ndipo uyenela kumakumbukila kuti ukamapanda akutsatila za kuno Malo Ako ogona thupi lako ndi imwewa"

"Musadandaule kalikose ndizatsatila chilichose chomwe mungatiuze pofuna kukusangalatsani mfumu "

Anayamba kuyendeka galimoto yopuma Jane ndipo osanama zinayamba zinthu kumundela kwambili

"Jane apatu mwafikapo tsopano Kodi muzikhalabe ndi ine kapena mupeza nyumba"

"Aaan ayi Melissa inetu ndikufuna kupitiliza kukhala ndi iweyo"

"Mmmm komatu ukuyenela kudziwa kuti kufunika kukhala pawekha kuti chuma chako chichiluke"

"Oooh Kodi nde tipezeleni nyumbayi"

"Nyumbayi Yako Ili kale ndipo anakupsa utangojoina gulu lathuli"

Anapita kukamuwonetsa nyumba yomwe amayenela kukhalayo ndipo inali nyumba yafanana ndendende ndi imene Melissa amakhala

Anayamba kukhala ekha Jen ndipo zomwe zimapangikazi zimangomusangalatsa

Tsiku linna anafuna ku kuwasangalatsa akulu akulu akugulu kwakeko ndipo anaganiza zopeleka nsembe asanauzidwe.

"Hello mwasowatu aunt zikutheka koma"

Munanveka mawu a Jennifer nyumba mwa aunt ake pamene makolowa onse awili amadya chakudya chamadzulo apa tsikuli

Nkhani ikupitilila

Ndi 500 kwacha yokha pa mwezi anzanu akuwelenga ma story awili pa tsiku ku Whatsapp if interested Whatsapp me on 0993222379

Address

Area 24
Lilongwe

Telephone

+265993222379

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Calvin top 10 love stories posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share

Category