16/04/2026
Mtsogoleri wa mpingo wa ECG Mneneri Shepherd Bushiri walamula ma Lawyer ake kuti atengere ku bwalo la mlandu a Peter Sambo chifukwa cholemba nkhani zabodza ndi zowanyoza, zomwe akhala akulemba pa makina a intaneti maka kudzera pa Facebook.
Mlanduwu udzamvedwa ku Khoti Lalikulu ku London, ku United Kingdom, ndipo zotsatira zake ngati atapezeka olakwa zikhoza kukhala zolamitsa kwambiri.
Iwo ati alamula gulu lawo la maloya ku UK kuti ligwiritse ntchito malamulo pofuna kuti nkhaniyi ifikire kwa a nthambi yowona zolowa ndi kutuluka mdzikolo, ya immigration, kuti pempho la bambo Sambo lofuna kuwonjezera zikalata zawo zowayenereza kukhara mdzikoro liwunikidwe mosamala potengera khalidwe lawo.
Malamulo a ku UK amaona ngati munthu angakhale chiopsezo kwa anthu ena, ndipo kunyoza (defamation) kumatengedwa ngati mlandu waukulu. Mneneli Bushiri watiso akudziwa kuti a Sambo ali ku UK pa visa ya ukwati ya zaka ziwiri ndi theka, ndipo pempho lililonse lomwe akupanga kapena adzapange lidzawunikida mosamala ndi abwalo.
Iwo awonjezera kunena kuti zomwe tikufuna ku Khoti Lalikulu ku London n’zosavuta, pomwe a Sambo akhoza kudzapereka chindapusa cha ndalama zokwana £50,000 chifukwa cha kuwononga mbiri yanga. Ngati angalephere kulipira, malinga ndi lamulo la Attachment of Earnings Act 1971, bwalo likhoza kudzalamula kuti ndalamazi zizidulidwa pa malipiro awo mpaka ngongole itatha. Ngati izi zingadzafike apa, ndidzalandira chindapusa chimenecho mokondwa.
Mneneli Bushiri wati monga ndakhala ndikunenera mmbuyomu, ndidzagwiritsa ntchito njira zonse zovomerezeka pofuna kudziteteza. Ichi sichiwopsezo, koma kudzipereka kutsata chilungamo kudzera m’malamulo oyenera.
Kuphatikiza apa, maloya anga akulumikizana ndi mabwana awo pankhaniyi.
A Bushiri anawonjezera kunena kuti zakhala zomvetsa chisoni kuwona kuti anthu ena akachoka ku Malawi kuno, nkupita kunja, akumayamba kunyoza ena omwe ali kuno kumudzi, poganiza kuti sangazengedwe milandu, koma pano sizili choncho kwa ine chifukwa ndidz