11/09/2026
Tijoyineni pa Gulu la Whatsapp lathu potumiza mawu akuti "Add me" ku nambala iyi: +265985105580
📝 NKHANI 📝
CHISANKHO CHA KENEDE
Yolembedwa ndi Micah Kanyenda
Unali masana, dzuwa likuswa mtengo, kukutentha ngati mng'anjo ya moto pamene mudzi wa Chimutu unawona mazangazime ndi masalamusi. Kenede ananyonyomala pansi pa mtengo mu nkhalango ya m'mudzimo, thupi lake litagwidwa tsembwe, akupumira mwamba ngati galu wachiwewe. Iye anabisala kufuna kuwonetsetsa ndi kumvetsetsa tsoka lomwe linabwera m'mudzi mwawo mwa bata ndi mtendere muja. Anamva kulira kwa chikwanje.
"Ifetu mukangomutulutsa Man Chiyo basi mudzipulumutsa nokha, apo bi! Muona chimene chinameta nkhanga mpala. Ndiwerenga katatu, ndipo kachitatu ngati simukuyankhabe ndikhapa uyu" Analankhula m'modzi wa anyamata amene anadzitseka kumaso ndi chinsalu chakuda, uku akudzutsa m'modzi mwa anyamata a m'mudzi wa Chimutu, Tomasi.
Kenede anapatula masamba a mtengo amene anatchinga maso ake kuti awonetsetse malodza amene amavumba m'mudzi mwake. Anawona anthu owoneka moopsya, ovala zotchinga kumaso, zikwanje zili waliwali zonola, zowala ngati nyenyezi zili m'manja. Patali choncho anawona Tamika, Belita ndi Tomasi ndi ena anzake atagwada, nkhope zawo zitazgolika, matupi awo atamera mphepo, akunjenjemera mu dziwe la mantha.
"Ndikufunsa komaliza, Man Chi ali kuti?" Anafunsa m'modzi wa iwo, nkhope yake itakwinyika ndi ukali, maso ali psuuu ngati mwalowa moto.
"Sitinamuone, tikunena chilunga......"
"1.............2..............3"
Nthawi yomweyo mlendo uja anaponya chikwanje mwankhaza, ndipo anakhapa m'mutu Tomasi. Magazi anamwazika ndikugwera kumaso kwa wokhapa uja komanso amnzake a Tomasi aja. Mutu mwa Tomasi munatemeka ndipo panali dzenje lalikulu lomwe limatulutsa mpopi wa magazi. Tomasi anagwa pansi, uku akuthatha m'mapumidwe, moyo ukutsanzika. Kenede analira mosisima, mwamatha ndi mosweka mtima, chifukwa amaona zonse zikuchitika. Kenako chigawenga chinakhapa Tomasi chija chinagwira Tamika, msungwana woyererapo pang'ono, chiphadzuwa cha m'mudzi mwa Chimutu, wa nkhope yosalala ngati thupi la mwana.
"Ndikubwerezanso, ndiuzeni kumene kuli Man Chi" Anafunsanso akupukuta magazi pa chikwanje chija, kukonzekera kuti apitilize chiwembucho.
"Sitimamudziwa, sakhala m'mudzi uno!" Anafuula Tamika, misozi ili pupupu!
"Ndekuti anthu atiwuza za mudzi uno ndi amisala?" Anafunsa m'modzi wa iwo. "Kuti mudziwe kuti sitinabwerere ntchedzero pano, muchimina nonse."
Pompo wina anatenga chikwanje, ndikuvunga mwamphavu. Anthu onse analira mopfuula.......
"Chonde mukafunse m'nyumba....... ya pakonayo, imene ili ndi utoto wobiliwira" Anasisima Tamika , mawu ake anali ali muukonde wamantha "Chonde chonde musandiphe!, Ife kuno sitimudziwa"
"Musamalitsetu! ngati sitimva nfundo yogwirika mnyumba imeneyo lero nonse mubyala chinangwa." Anakalipa winanso wovala zotchinga kumaso.
Belita ndi Tamika analira mokweza, namugwira Tomasi kuyesa kumupulutsa. Panali nyanja ya magazi imene imachoka m'mutu mwa Tomasi pamene gulu la zigawengazi limalowera ku nyumba ya pakona kumene amati akamve za Man Chi.
Mobisa Tamika anatenga lamya yake, nkuyimbira a Police a mderalo kupempha chipulumutso.
Nthawi yomweyo Kenede anavumbuluka kuti akathandize anzake. Chongotuluka mu nkhalango nkufika pa khomo loyamba, anawona mwana wa m'manja, atatemedwa dzanja akungolira. Kenede anayima, kutenga nsalu yina yomwe inali pachingwe, nkumumanga kuti magazi asatuluke ambiri. Mtima wake unawawa kwambiri. Kulira kunali kumveka ponseponse. Chisoni chinali chitakuta mudzi wonse wa Chimutu.
"Sinoya! ....Sinoya.......Sinoya mwana wanga!" Anamva kulira kuseli kwa nyumba yomwe iye anali. Mawuwo adamukhadzula mtima chifukwa anazindikira kuti ndi mayi ake Nachanza. Pompo anathamangira komweko kuti akamve chakuda chomwe chamuwona mng'ono wake Sinoya.
"Amayi, Sinoya watani? Ali kuti?" Anafunsa mayi ake omwe anali kusamba misozi, atagwilira chitenje m'chiuno.
"Amayeee amayeee! Ndikungomva kuti wakhapidwa ndipo wakabisala mnyumba ili pakonayo. Moyo wake uli pa chiswe poti zigawengazo zalowera konko. Chonde chonde thamanga kapulumutse m'ngono wako mwana wanga Kenede" Anapfuula mayi ake.
Nthawi yomweyo Kenede anayamba kuthamangira ku nyumba ya pakonayo. Kenako anawaona anyamata aja, atamugwira Sinoya, akumukhwekhweza.
Kenede anagwidwa ndi mantha aakulu. Pompo anazemba nathawira patchire, phone ili m'manja. Apa mayi ake anagwa pansi akulira.
"Chonde Kenede, usathawe, m'bale wako aphedwatu!" Analira mayi ake.
Kenede analiyatsa la mtondo odooka kulowera patchire, Kenako anatulutsa lamya nkuyika kukhutu.
"Bwana, bwana! Chonde tikufa kuno. M'mudzi mwathu mwabwera nkhondo. Zikukhala ngati akudzabweza chipongwe chija. Chonde tithandizeni!" Analira.
"Nde ndithandize motani popeza anyamata anga omwe ndimadalira ndi inuyo?Onetsani mphamvu, pano palibe ndingachite!" Anamveka kung'alula bwana wa Kenede. Mawu awo anamutsutsula chilonda Kenede.
"Bwana simungatitumizire mwana wanu Trevor kuti adzangowaophyeza ndi mfuti? Sizili bwino bwana, madzi achita katondo!"
"Napepe nzosatheka. Ndikunena pano Trevor wakwera ndege dzulo, wabwerera ku school ku America" Anayankha bwana.
"Nanga nde ti........
Lamya inaduka. Anayesera kuyimbanso Koma sinagwirenso.
Kenede anazindikira kuti ndi bwana wake chinali chikondi cha nkhwanga, chokoma pokwera. Mwachisoni anayamba kunong'oneza bondo povomera kukachita za upandu ku misonkhano yachipani china yomwe imayenera kuchitika pafupi ndi m'mudzi mwa Chimutu. Ngakhale anali atalandira dipo, analakalaka kuwasanza makobiliwo, popeza sakanathanso kuteteza nawo miyoyo ya azinzake.
Apa panalibenso kuchitira mwina, anadziwa kuti yalimba nkandiro, ng'ombe zayang'ana ku ngolo.
"Palibenso njira Ina, koma kungovomereza, ukaziputa limba basi." Ananong'ona
Kenede anavala chotchinga kumutu naye, nabwerera kuti akapulumutsa m'ngono wake ndi ena.
"Ndikubwerezanso! Pa nyumba ya pakonayo tapeza uyu ndipo sakukamba zogwirika. Ife tati tikufuna Man Chi, osati timanjolinjoti. Nde poti simukufuna kutiwuza, uyunso tikupha. ndiwerenganso katatu" Analankhula mnyamata okhapa uja, uku akumukoka Sinoya, magazi akudontha kukhutu kwake.
"Chonde chonde musamuphe! Chabwino, Iphani ineyo! kaya mukuti Man Chi mukufunayo siwa m'mudzi muno chonde" Analira Nachanza, atagwada pafupi ndi mnyamata okhapa uja.
"Inuyo masteni sizikukhudzani. Apa siza nkuyu zodya mwana, nkupota wamkulu ayi. Uyu wakula watha, aziwona, kufa saferana.
Ndiyambanso kuwerenga 1......... 2.........3
Pompo anakweza chikwanje m'mwamba, nthawi yomweyo munthu wina wovala chotchinga kumaso chobiliwira anawankha.
"Ndabwera, siyani kupha anthu m'mudzi mwanga muno." Analankhula Man Chi.
Chodulitsa mutu wa zizwa kwa Anachanza chinali choti mawuwo sanali achilendo kweni kweni. Nthawi yomweyo kunavungidwa mpeni, omwe unafikira ndikubaya pamimba pa Sinoya.
Man Chi anamugwira Sinoya, mtima wake uli osweka, anazulapo mpeni uja, Sinoya anayamba kubanika popuma. Man Chi anavula malaya kumanga pa mimba pa Sinoya uku misozi ikugwa ngati mvula.
"Ndakuwuzani kuti ndabwera, chimene mukuphera mng'ono wanga ndi chani?"
"Kenede?" Anafunsa modabwa Anachanza, nawo misozi itadzadza pa nkhope. Thupi lonse lili ndi magazi.
"Amama, .......ama khululukuleni, Man Chi amasakidwayo ndi ineyo, ndimatumidwa ndi bwana MP. Ndazindikira nkhwangwa ili m'mutu kuti ndinali wogwiritsidwa ntchito chabe, chida chosula tsogolo lawo." Anayankha, misozi ili pupupu!
Pompo anavunga chikwanje chija ndipo chinafikira kumaso kwa amene anabaya Sinoya uja. Anzake a mnyamatayo anamuwunjikila Kenede ndi zida zawo zokuthwa.
"Ntchito ....zanga zandibwerera" Kenede analira ngati nkhanda lobayidwa kumene katemera, zoti amavutitsa ngat Man Chi, sizinaphule kanthu. Sadyeka anali akudyeka ndi mafupa omwe. Chisankho chake, chinamuyika m'mavuto. Magazi anali posepose pamene galimoto ya apolisi imafika.
[MATHERO]
***** ***** ***** ****** *****
M***a kulumikizana ndi mlembiyu pa: +265993097689
Tiuzeni maganizo anu ndi momwe mwayimvera nkhaniyi. Yamikirani kapena kudzudzula mfundo zake komanso kalembedwe kake. Chongani nkhaniyi kuchokera pa mlingo wa 10.
Tumizani nkhani zanu ku:
Page Inbox/WhatsApp: +265985105580
GOODWRITES LITERATURE
Bwalo la a Malawi Olemba ndi Owerenga.
Copyright © 2026
Malamulo Onse Asungidwa!
POST YATHU YOTSATIRA ⏭ Maphunziro [Phunziro 1: Mitundu ya Mawu (Gawo 11B/12: Mitundu ya Aphatikiri)], @ 3:00 P.M.