Bwalo la alakatuli by mr.ojegwe poet

Bwalo la alakatuli by mr.ojegwe poet Nkhani za chikondi(mr ojegwe)

@@ LOVE STORY@@@ ..............LOADING........
25/04/2021

@@ LOVE STORY@@@

..............LOADING........

19/04/2021

@@ CALL ME BACK@@ 2........ Choyamba pangani like page lathu.

Previous...
Martin adagwesa misozi yamatalala atawona nkazi wake walimba ntima kumapita kwawo,chonde hny usandithaweeee....

Next...
Martin analira nthawi yaitali anga chikalambile kulilira katundu wake utapsa,koma palibe chinasintha.hello! Hello! Martin kuli anthu kuno,uyu anali Fred nzake wa martin, yoooo ndilikuno man talowani,anayankha Martin Ali busy kuchapa zovala ubatchala utamuyanja.Nde nzanga uzipanga chani sopano pamene wagwera m'matope kawiri(waluza ntchito komaso nkazi wako)?Martin atangomva nkuluwiko wanzakeyu misozi inayamba kulengeza chifukwa anali atamukumbusa wachikondi wake wapadzana,basi man khalani ngati mamuna sik*tha kwaziko koma ndi chiyambi chamoyo wina.Fred anamulimbikisa nzake ndipo anayankhula bwino ngati pa maliro.

Patatha mwezi umozi(a month later)Martin anapitaso ku company komwe ankagwira ntchito akawone k*ti zili pati.hello guys mulibwanj?wathanzi malume,uyu anali Martin kulonjera azizake omwe ankagwira nawo ntchito padzana.guys ndikupezani ndikumane Kaye ndi abwana,eeeee Martin dikira Kaye ndikuganiza k*ti kupita kwa abwana pakadali pano siganizo labwino chifukwa kuli bomba ukachoka kumeneko phulusa lokha lokha,uyu anali gibo kuyankhula ngati mwina Pali chinachake chomwe akubisa.bwanji Pali chomwe ukufuna kundiuza kapena??anafusa Martin modabwa,ai palibe ndangokuchenjeza monga nzanga.ok osadandaula gibo abwana sitingadane poti anandichosa ntchito,anayankha Martin momwetulira uku akulunjikira ku office ya abwana ndipo azizake onse anangoti kukamwa yasa anga aluma dowe wothira nsabola.Martin atayandikira office anamva kuyankhulana kwa anthu awiri kwinaku sound ya kiss ikumveka k*ti mwaaa mwaaa chiseko chili chosegula,Martin anaima Kaye naganiza zobwelera ,Ali pachiseko pompo ding ding ding phone ya abwana inalira ndipo anamva abwana ake akuyankha phone pompo anapezerapo mwayi nalowa .heeeee Martin chongolowa maso ndi maso ndi nkazi wake Brenda....ikupitilira

2020 NDIWE CHIZELEZAInde yenda bwino upitako 2020 watikwana anga mayeso ausilikali.Tidakuzindikira mochedwa sudabwelere ...
17/04/2021

2020 NDIWE CHIZELEZA

Inde yenda bwino upitako 2020 watikwana anga mayeso ausilikali.
Tidakuzindikira mochedwa sudabwelere mtendere koma k*titapa nkamwa.
Tisakulangize, uwooo wako nkwiyo ndk*tipasa kanganya wometa m'mbali covid-19.

Tisaname watibera miyoyo yochuluka ndpo aliyese alibe mawu paiwe.
Ai ife tagonja matako m'mwamba manja akulenga yenda bwino.
Inde tikuziwa wakuba sapanga retire koma inu nokha kapumeni mwakula malume 2020.

Ndithudi zoti mphuno ndi pakamwa ndi Malo obisika ai taphunzira kwainu malume.
Ana anthu abwino aja mimba atenga atengaso anga katemera wa chiwewe.
Ndagoma ine mwana ntsikana mimba kukatenga PA mwezi katatu anga ngongole yakatapila.
Ulemu ngwanu nsanje to chitipa mwapambana 2020.
Ndipo mbiri yanu tizaika PA front page mu history ya dziko lino mumakwana.

Ambiri akwatira asakufuna siukatakwe koma kuwopa kufa asanabelekeko.
Maiko akuvulira chipewa manja mchiuno Na corona anakonza.
Mayeso omwewa mpaka kulemba kawiri anga nyamata woiputa dala mitala.
Komano usanapite taima Kaye Tati tikuwombere m'manja wapanga chanzeru.
Anthu anali otaika koma kamba kaiwe corona taziwa kupita ku tchalitchi namusata ambuye.

Eeeeee koma Na iwe aliyese wavomeleza k*ti anakonza corona.

2020 NDIWE CHIZELEZA............Clarence chiku Banda.....

17/04/2021
14/04/2021

@@ CALL ME BACK@@ 1....choyamba pangani like page lathu .ngiliiiiiii(alarm ringing) hny tazuka kodi lero sindisamba popita ku ntchito?martin adafusa atavumbuluka pa k**a lake ,ndipo nkazi wake sanayankhe chinachilichose m'malo mwake anali akukokera gombeza kwakuya tulo titakoma.Martin:hny basi ndapita
Brenda:chabwino usaiwale kundiikira ndalama ya ku saloon patebulopo.Martin mwakachetechete anaika ndalamazo namapita ku ntchito.

Ili linali banja la Martin ndi Brenda.Martin anali nyamata wozichepesa komaso wochezeka pamene nkazi wake Brenda anali womva zayekha nkaz wosaziwa mavuto,womangolota ndalama akakhala eeee Martin anakwatira mavuto.

Martin atafika ku ntchito mwachizolowez anatenga worksuite ati azivala,Martin ! Martin !akukuitana abwana ,mwamachawi nkului anathamangira komwe anaitanidwako,Martin :ndamva kuitana abwana.
Boss:eya ndne ndakuitana eko kalatai.
Martin:mulichan mukalata abwana ?
Boss:pepa kwambir Martin company yathu sikupindula nde taganiza k*ti antchito ena tichoseko Kaye tizakuitanisani zikalongosoka.
Martin:chonde abwana msandpange zimenezi nanga ndilowera k*ti komatu ndili ndi banjatu ine komaso ndangokwatira kumene.

Martin anayesesa kugwada koma sizinaphule kathu ndipo ananyamka sapato mumanja kubwelera kunyumba,msaiwale mavuto akakugwera chilichose chimakulemera.

Hny chavuta ndchan ?Brenda adafusa modabwa ngat mwina wawona mbuzi ikuguza ngolo,m'malo motankha anangompasa kalata nkaziwakeo k*ti awone yekha chomwe chapangisa abusa k*tukwana neba zamu kabudula.

Brenda atangothila diso tanthauzo la kalatao analunjika kuchipinda napakila zovala zake kumapita kwawo uku akugeya mwano "singakhale ndi mamuna wokanda ". Martin anagwesa misoz atawona nkaz wake walimba ntima kumapita kwawo.hny chonde usandithaweeee....ikupitilira chonde ma comment Anu ndomwe ndilimbikise ine zikoma azizanga osaiwala kupanga like page lathu

14/04/2021

@ CALL ME BACK@ 1 typing........

04/12/2020

Hello people eeee koma nde tasowana guys koma osadandaula kukubwera akhatundu johan yabwino kwabas mngoyembekeza pangono guys

Send a message to learn more

๐Ÿ’ฅDONT BLAME ME Part 4๐Ÿ’”๐Ÿ’”๐Ÿ’”๐Ÿ’”choyamba pangani like page lathu. Tiyeni nayoni nkhani yokomai. Previous๐Ÿ‘‡Pa 1 January 12:00am p...
24/07/2020

๐Ÿ’ฅDONT BLAME ME Part 4๐Ÿ’”๐Ÿ’”๐Ÿ’”๐Ÿ’”choyamba pangani like page lathu. Tiyeni nayoni nkhani yokomai.

Previous๐Ÿ‘‡
Pa 1 January 12:00am phone inalira ine hello ๐Ÿ‘‹ ndindani? Ndine Sandra ndakusowa wachilowa bwanj chaka? Ine..????

Next๐Ÿ‘‡
Ndinali wodabwa pomwe Sandra munthu wot takhala mwezi osayankhulana ndikumandiuza k*ti wandisowa, ndisaname chakachi ndinachilowa ndisangala za pusi,

Kutacha mamawa ndinalandira phone yake nkumanduza k*ti tikumane sinaphwekese koma kusamba mwachangu maso kunsewu, mosakhalisa anatulukira ndipo zinali zokoma tinacheza ngat chibwez chatha zaka 4.

Patapita masiku ndithu nditafasa foni inazalira ine ndiwone nkupeza k*t SMS ikuchokera kwa memory(i'm ready now to give you my heart) ndinagwidwa shock nthaw yomweo ndinasokomora nafuula ndipaseni madzi ndingakomoke palibe anandiyankha, ndinaiwala k*t pamalopo ndinalipo ndekha.

Koma poti ndinaziyamba ndekha sinampange chipongwe koma kumsangalalira, eeee abale anzanga atsikana awiriwa anandpasa ukhuluku chifukwa ndnkafuna aliyese azisangalala, zibwez zanga zinkayenda bwino kwambir ndisaname nthaw ndinkaigawa bwino kwawosewa.

Sandra ndinamuza k*ti tizikumana Saturday pamene memory tinkakumana nkat mwa week ndipo palibe yemwe ankandikaikira chifukwa zofuna zawo komaso nthaw yantsikana ndinkaipeleka mokwanira.

Pa 15 January tinatengana ndi Sandra wawutali ku don bosco kukacheza, tinadzera kungwenya kuwopa k*t memory asatiwone chifukwa anthu onsewa anali ansanje. Tili nkati mocheza, "tabwera ndikudyese sweet"anatero Sandra momwetulira atapenga ndi chikondi, ding ding foni inalira, nditawona anali nzanga zinali motere:
Joe:hello kanganya
Ine:mwati bwanj Mikozi
Joe:ankolo kwabwera Ethel ku shop kuno ati akukufuna.
Ine:zoona?? Ak*ti akundifunilanj ankolo anga?
Joe:Mmmmm wakana kunduza ak*ti ndizokhuza iweo ndine bas nde amandfusa k*ti mulik*tiko
Ine:nde mwamuza k*ti chan ankolo?
Joe:ndangomuza k*ti wapita kwawo kukasamba.
Ine:ok chabwino ankolo osamuza komwe ndapita ndili naye ngongol. Ikupitili

DONT BLAME ME part 3๐Ÿ‘‡๐Ÿ’”๐Ÿ’”๐Ÿ’”choyamba pangani like page lathu. Previous ๐Ÿ‘‡Ding ding ding phone inalira mosachedwa ndinatenga p...
01/07/2020

DONT BLAME ME part 3๐Ÿ‘‡๐Ÿ’”๐Ÿ’”๐Ÿ’”choyamba pangani like page lathu.

Previous ๐Ÿ‘‡
Ding ding ding phone inalira mosachedwa ndinatenga phone k*ti ndiwone ndindani(SMS:ndikusonkha moto tabwera sindikwanisa popanda iweyo).

Next๐Ÿ‘‡

Message ๐Ÿ’ฌ yomwe inandipeza inandipasa maganiza ndipo sinachedwe ndnafusa uk*thandauzanji? Sanandiyankhe. 3 weeks later anazanditumizila SMS yomwe k*ti message ija sinali yako, zinandikhuza kwambiri ndipo ineso sinayankhe or mtakhala inu mngatani?

Tsiku lina litafasa monga muziwa maluzi akusweramu, panazabwera tsikana winawake kuzaikisa film mosapindila ndevu nkamwa ndinawonesa chamuna musaiwale paja ndilibe chibwez. Nditamfusa bwinobwino nkazi uja ananduza k*ti nzina lake ndi memory, amakhala ndi agogo ake k*tereku holiday ikatha abwelera ku xul. Memory anali mwana wa ulemu tinamvana bwinobwino koma ananduza k*t andiyankhabe andifufuze kaye sinapange phuma koma kusata Khumbo lake.

Patapita masiku atatu ndnamva zoti memory wabwelera ku xul zinandivuta kukhala ndipo tsokali linandikulira ndikaganizira Sandra komaso memory.

Komabe sinagive monga muziwa life ya anyamata ometa m'mbali zimafunikabe utakhala ndikenakake kokukanda pa danzi. Ndinakumbukira tsikana yemwe m'maganizo anga munalibemo ndipo most of times I used to sent her kwa azizake owonekako bwino, nkaziyu ankandifuna koma paja nkaz zimamvuta k*tulusa chichewa. Dzina lake anali Ethel ndipo nditamubenthulira nkhawa zanga sanandibisire koma kunduzitsitsa ka chilungamo kobaya ati ndine wanchiwuno.

Eeeee abale anzanga ndinkawona ngati ziphwekerako poti amandifuna ndikale koma likakuwona litsiro mvura siikata. Ndinatha week ndkunyengelerabe ndipo nayeso ananduza k*ti andiyankhabe.

Patapita week mmm ndinagiva zoti ndizakhalaso ndi chibwezi, zanga phee osaganizakoso zankaz. Tsiku lomwe lokoma lomwe anthufe timayembekezera la Xmas ๐ŸŽ„ linadusa ine ndlibe chibwezi ndithu.

Pa 1 January 12:00am phone inalira ine hello ๐Ÿ‘‹ ndindani? Ndine Sandra ndakusowa wachilowa bwanj chaka. Ine..??ikupiti

๐Ÿ“๐Ÿ“ADDICTED TO S*X..... Part 1 ๐Ÿ“๐Ÿ“๐Ÿ“๐Ÿ“
10/06/2020

๐Ÿ“๐Ÿ“ADDICTED TO S*X..... Part 1 ๐Ÿ“๐Ÿ“๐Ÿ“๐Ÿ“

Address

Area 23
Lilongwe

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Bwalo la alakatuli by mr.ojegwe poet posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share

Category